Koma ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi nyama yace, ndi cipwidza cace, anazitentha ndi mote kunja kwa cigono; monga Yehova adamuuza Mose.