Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, ciwacokere ku nsembe zamoto za Yehova; ali yense wakuzikhudza izi adzakhala wapatolika.