1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2. Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Munthu akacimwa, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Mulungu, nakacitapo kanthu;
3. akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kuparamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita, ikhale nsembe yaucimo.
4. Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la cihema cokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lace pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.
5. Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwerenao ku cihema cokomanako;
6. ndipo wansembeyo abviike cala cace m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova cakuno ca nsaru yocinga, ya malo opatulika.