40. azikhala nawe ngati wolipidwa nchito, ngati munthu wokhala nawe; akutumikire kufikira caka coliza lipenga.
41. Pamenepo azituruka kukucokera, iye ndi ana ace omwe, nabwerere ku mbumba yace; abwerere ku dziko lao lao la makolo ace.
42. Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.
43. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.
44. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo amuna ndi akazi.
45. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.
46. Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.
47. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera cuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa pfuko la banja la mlendo;
48. atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ace amuombole;
49. kapena mbale wa atate wace, kapena mwana wa mbale wa atate wace amuombole, kapena mbale wace ali yense wa banja lace amuombole; kapena akalemera cuma yekha adziombole yekha.
50. Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.
51. Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndarama zakumuombola zocokera ku ndalama zomgulazo.