1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti,
2. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.
3. Zaka zisanu ndi cimodzi ubzale m'munda mwako, ndi zaka zisanu ndi cimodzi udzombole mphesa zako, ndi kuceka zipatso zace;
4. koma caka cacisanu ndi ciwiri cikhale sabata lakupumula la dziko, sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako.
5. Zophuka zokha zofikira masika usamazichera, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usaziceka; cikhale caka copumula dziko.