17. Munthu akakantha munthu mnzace ali yense kuti afe, amuphe ndithu.
18. Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere yina; moyo kulipa moyo.
19. Munthu akacititsa mnansi wace cirema, monga umo anacitira momwemo amcitire iye;
20. kutyola kulipa kutyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anacitira munthu cirema, momwemo amcitire iye.
21. Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere yina; iye wakupha munthu, amuphe.
22. Ciweruzo canu cifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.