2. koma cifukwa ca abale ace eni eni ndiwo, mai wace, ndi atate wace, ndi mwana wace wamwamuna, ndi mwana wace wamkazi, ndi mbale wace;
3. ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.
4. Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wace, asadzidetse, ndi kudziipsa,
5. Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kucecerera ndebvu zao, kapena kudziceka matupi ao.
6. Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; cifukwa cace akhale opatulika.
7. Asadzitengere mkazi wacigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamcotsa mwamuna wace; popeza apatulikira Mulungu wace.
8. Cifukwa cace umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera,
9. Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kucita cigololo, alikuipsa atate wace; amtenthe ndi moto.
10. Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ace, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pace, amene anamdzaza dzanja kuti abvale zobvalazo, asawinde, kapena kung'amba zobvala zace.