wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndebvu.