Koma wansembe akaciona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sicinakumba kubzola khungu, koma cazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;