Coipa cao conse ciri m'Giligala; pakutipamenepo ndinawada, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe ao ndidzawainga kuwacotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.