Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kuturuka kwace kwakonzekeratu ngati matanda kuca; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.