Ndipo ndidzamlanga cifukwa ca masiku a Abaala amene anawafukizira, nabvala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zace, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.