1. Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wocitidwa-cifundo.
2. Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo acotse zadama zace pankhope pace, ndi zigololo zace pakati pa maere ace;
3. ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
4. ndipo ana ace sindidzawacitira cifundo; pakuti iwo ndiwo ana acigololo.
5. Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.