1. Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoto.
2. Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;Yehova, tsitsimutsani nchito yanu pakati pa zaka,Pakati pa zaka mudziwitse;Pa mkwiyo mukumbukile cifundo.
3. Mulungu anafuma ku Temani,Ndi Woyerayo ku phiri la Parana.Ulemerero wace unaphimba miyamba,Ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
4. Ndi kunyezimira kwace kunanga kuunika;Anali nayo mitsitsi ya dzuwa yoturuka m'dzanja lace.Ndi komweko kunabisika mphamvu yace.
5. Patsogolo pace panapita mliri,Ndi makara amoto anaturuka pa mapaziace.
6. Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;Anapenya, nanjenjemeretsa amitundu;Ndi mapiri acikhalire anamwazika,Zitunda za kale lomwe zinawerama;Mayendedwe ace ndiwo a kale lomwe.