Nuike cikho canga, cikho casiliva ciija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zace. Ndipo iye anacita monga mau ananena Yosefe.