8. Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwace. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwace, namupha,
9. Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?
10. Ndipo anati, Wacita ciani? Mau a mwazi wa mphwako andipfuulira Ine kunthaka.
11. Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, Imene inatsegula pakamwa pace kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako:
12. pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yace: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.