1. Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isake ananka kwa Abimeleke mfumu ya Afilisti ku Gerari.
2. Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Aigupto, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;
3. khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa cilumbiriro ndinacilumbirira kwa Abrahamu atate wako;
4. ndipo ndidzacurukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;