Ndipo Abrahamu anatukula maso ace nayang'ana taonani, pambuyo pace nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zace m'ciyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wace.