26. Ndipo anati Abimeleke, Sindinadziwe amene anacita ico; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.
27. Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleke, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.
28. Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri pa okha.
29. Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Nanga ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?
30. Ndipo anati, Ana a nkhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine citsime cimeneci.
31. Cifukwa cace anacha malowo Beereseba: cifukwa pamenepo analumbira onse awiri.
32. Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa-nkhondo yace, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.
33. Ndipo Abrahamu ananka mtengo wabwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.