Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakucitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe citseko.