Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umcitire iye cimene cikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwace.