Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ace, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.