Limodzi la magawo ace atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapula-kwapula ndi lupanga pozungulira pace, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.