Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zocuruka zidzakhala ndi moyo kuti konse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzacuruka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kuli konse mtsinje ufikako ziri zonse zidzakhala ndi moyo.