Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinacititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinacepsa mitsinje yace, ndi madzi akuru analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebano, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota cifukwa ca uwo.