M'codetsa cako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukucotsera codetsa cako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.