Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakucitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakucotsera ana ako amuna ndi akazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.