Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kucotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo cicitike monga mwa cilamulo.