Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.