21. Utali wace wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwace kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.
22. Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a kacisi.
23. Ndipo anapanga matabwa a kacisi; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwela, kumwela;
24. napanga makamwa makumi anai pansi pamatabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri.