8. ndi gomelo ndi zipangizo zace, ndi coikapo nyali coona ndi zipangizo zace, ndi guwa la nsembe lofukizapo;
9. ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace;
10. ndi zobvala zotumikira nazo, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakucita nazo nchito ya nsembe;
11. ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca zonunkhira zokoma za malo opatulika; azicita monga mwa zonse ndakuuza iwe.
12. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
13. Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.
14. Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; ali yense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti ali yense wakugwira nchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wace.
15. Agwire nchito masiku asanu ndi limodzi; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; ali yense wogwira nchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.
16. Cifukwa cace ana a Israyeli azisunga Sabata, kucita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;