Muka, nukasonkhanitse akuru a Israyeli, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, ndi kuti; Ndakuzondani ndithu, ndi kuona comwe akucitirani m'Aigupto;