19. Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.
20. Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
21. Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.