Ndipo uzipanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, nchito ya mmisiri.