19. Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulira-kulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.
20. Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pace pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo.
21. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, cenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.
22. Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.
23. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwaticenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula.
24. Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika: nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.
25. Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.