13. Ndipo Yoswa anatyola Amaleki ndi anthu ace ndi kuukali kwa lupanga.
14. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ici m'buku, cikhale cikumbutso, nucimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse cikumbukilo ca Amaleki pansi pa thambo.
15. Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalicha dzina lace Yehova Nisi:
16. nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleki m'mibadwo mibadwo.