3. Yehova ndiye wankhondo;Dzina lace ndiye Yehova.
4. Magareta a Farao ndi nkhondo yace anawaponya m'nyanja;Ndi akazembe ace osankhika anamira m'Nyanja Yofiira.
5. Nyanja inawamiza:Anamira mozama ngati mwala.
6. Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.
7. Ndipo ndi ukulu wanu waukuru mwapasula akuukira Inu;Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati ciputu.
8. Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
9. Mdani anati,Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha;Ndidzakhuta nao mtima;Ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.