ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kucita zoona pamaso pace, ndi kuchera khutu pa malamulo ace, ndi kusunga malemba ace onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aaigupto sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuciritsa iwe.