Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kucipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israyeli anakwera kucokera m'dziko la Aigupto okonzeka.