17. Pasakhale mkazi wacigololo pakati pa ana akazi a Israyeli, kapena wacigololo pakati pa ana amuna a Israyeli.
18. Musamabwera nayo mphotho ya wacigololo, kapena mtengo wace wa garu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, cifukwa ca cowinda ciri conse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
19. Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndarama, phindu la cakudya, phindu la kanthu kali konse kokongoletsa.