15. Musamapereka kwa mbuye wace kapolo wopulumuka kwa mbuye wace kuthawira kwa inu;
16. akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.
17. Pasakhale mkazi wacigololo pakati pa ana akazi a Israyeli, kapena wacigololo pakati pa ana amuna a Israyeli.
18. Musamabwera nayo mphotho ya wacigololo, kapena mtengo wace wa garu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, cifukwa ca cowinda ciri conse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.