1. Akapeza munthu waphedwa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha,
2. pamenepo azituruka akuru anu ndi oweruza anu, nayese ku midzi yomzinga wophedwayo;
3. ndipo kudzali kuti mudzi wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akuru a mudzi uwu atenge ng'ombe yamsoti yosagwira nchito, yosakoka goli;