Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.