Musamadya cinthu ciri conse citafa cokha; muzipereka ico kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, acidye ndiye; kapena ucigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.