30. Sakhala kodi tsidya lija la Yordano, m'tseri mwace mwa njira yace yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'cidikha, pandunji pace pa Giligala, pafupi pa mathunda a More?
31. Pakuti mulinkuoloka Yordano kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzacilandira colowa canu, ndi kukhalamo.
32. Potero samalirani kucita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino.