Koma ine, cinsinsi ici sicinabvumbulutsidwa kwa ine cifukwa ca nzeru ndiri nayo yakuposa wina ali yense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.