Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.