Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.