Ndipo Davide anakhala m'linga mula, nalicha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.