Pomwepo Yoabu anadza kwa mfumu, nati, Mwacitanji? Taonani, Abineri anadza kwa inu, cifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti acokedi.